1 Samueli 9:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo panali munthu Mbenlamlni, dzina lace ndiye Kisi, mwana wa Abiyeli, mwana wa Zerori, mwana wa Bekorati, mwana wa Afiya, mwana wa Mbenjamini, ndiye ngwazi.

2. Iye anali ndi mwana wamwamuna dzina lace Sauli, mnyamata wokongola; pakati pa anthu onse a Israyeli panalibe wina wokongola ngati iye; anali wamtali, anthu onse ena anamlekeza m'cifuwa.

3. Ndipo aburu a Kisi, atate wa Sauli, analowerera. Ndipo Kisi anati kwa Sauli mwana wace, Utenge mnyamata mmodzi, nunyamuke, kukafuna aburuwo.

4. Ndipo anapyola dziko lamapiri la Efraimu, napyola dziko la Salisa, koma sanawapeza; pamenepo anapyolanso dziko la Salimu; koma panalibe pamenepo, napyola dziko la Abenjamini, osawapeza.

5. Pamene anafika ku dziko la Zufi, Sauli anamuuza mnyamata amene anali naye, kuti, Tiye tibwerere; kuti atate wanga angaleke kusamalira aburuwo, ndi kutenga nkhawa cifukwa ca ife.

1 Samueli 9