1 Samueli 25:7-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Ndipo tsono ndamva kuti muli nao osenga nkhosa; abusa anu amene anali ndi ife, sitinawacititsa manyazi, ndipo panalibe kanthu kao kadasowa, nthawi yonse anakhala iwo ku Karimeli.

8. Mufunse anyamata anu, adzakuuzani; cifukwa cace muwakomere mtima anyamata awa, pakuti tirikufika tsiku labwino; mupatse ciri conse muli naco m'dzanja lanu, kwa anyamata anu, ndi kwa mwana wanu Davide.

9. Ndipo pakufika anyamata a Davide, analankhula ndi Nabala monga mau aja onse m'dzina la Davide, naleka.

1 Samueli 25