2. Nati Davide kwa Ahimeleki wansembeyo, Mfumu inandilamulira nchito, ninena nane, Asadziwe munthu ali yense kanthu za nchito imene ndakutumira ndi kukulamulira; ndipo ndawapanga anyamatawo ku malo akuti.
3. Cifukwa cace tsono muli ndi ciani? mundipatse m'dzanja langa mikate isanu, kapena ciri conse muli naco.
4. Ndipo wansembeyo anayankha Davide nati, Ndiribe mkate wacabe, koma ulipo mkate wopatulika; pokhapo ngati anyamatawo anadzisunga kupewa akazi.
5. Ndipo Davide anayankha wansembeyo, nati naye, Zoonadi tinafulatira akazi monga masiku atatu; cicokere ine, zotengera za anayamatawo zinali zopatulika ungakhale unali ulendo wacabe; koposa kotani nanga zotengera zao zikhala zoyera lero?