33. Ndipo Sauli anamponyera mkondo kuti amgwaze; momwemo Jonatani anazindikira kuti atate wace anatsimikiza mtima kupha Davide.
34. Pamenepo Jonatani anauka pagome wolunda ndithu, osadya kanthu tsiku laciwiri la mwezi, pakuti mtima wace unali ndi cisoni cifukwa ca Davide, popeza atate wace anamcititsa manyazi.
35. Ndipo m'mawa, Jonatani ananka kuthengoko pa nthawi imene anapangana ndi Davide, ali ndi kamnayamata.
36. Ndipo anauza mnyamata waceyo, Thamanga uzikatola mibvi Imene ndidzaponya; ndipo analikuthamanga mnyamatayu, iye anaponya mubvi kuutumphitsa iye.