1. Pamenepo Samueli anatenga nsupa ya mafuta, nawatsanulira pamutu pace, nampsompsona iye, nati, Sanakudzozani ndi Mulungu kodi, mukhale mfumu ya pa colowa cace?
2. M'mene talekana lero, mudzakomana ndi anthu awiri pa manda a Rakele, pa malire a Benjamini ku Zeliza; iwo ndiwo adzanena nanu, Aburu aja munakafuna, anapezedwa; ndipo onani, atate wanu analeka kulingalira aburuwo, koma alikulingalira za inu, ndi kuti, Ndidzacita ciani, cifukwa ca mwana wanga?
3. Mukapitirira pamenepo tsono ndi kufika ku mtengo wathundu wa ku Tabori, kumeneko adzakomana nanu anthu atatu akukwera kwa Mulungu ku Beteli, wina wonyamula ana a mbuzi atatu, wina mikate itatu, wina thumba la vinyo.
4. Iwowa adzakulankhulani, ndi kukupatsani mikate iwiri; imeneyi mudzailandira m'manja mwao.