1 Samueli 1:10-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Ndipo mkaziyo anali ndi mtima wowawa, napemphera kwa Yehova, naliratu misozi;

11. nalonjeza cowinda, nati, Yehova wa makamu, mukapenyera ndithu kusauka kwa mdzakazi wanu, ndi kukumbukila ine, ndi kusaiwala mdzakazi wanu, mukapatsa mdzakazi wanu mwana wamwamuna, ine ndidzampereka kwa Yehova masiku onse a moyo wace, ndipo palibe lumo lidzapita pamutu pace.

12. Ndipo panali, m'mene iye analikupempherabe pamaso pa Yehova, Eli anapenyerera pakamwa pace.

13. Koma Hana ananena mu mtima; milomo yace inatukula, koma mau ace sanamveka; cifukwa cace Eli anamuyesa woledzera.

14. Ndipo Eli anati kwa iye, Udzaleka liti kuledzera? cotsa vinyo wako.

15. Ndipo Hana anayankha, nati, Iai, mbuyanga. Ine ndiri mkazi wa mtima wacisoni; sindinamwa vinyo kapena cakumwa cowawa, koma ndinatsanulira mtima wanga pamaso pa Yehova.

16. Musamandiyesa mdzakazi wanu mkazi woipa; cifukwa kufikira lero ndinalankhula mwa kucuruka kwa kudandaula kwanga ndi kubvutika kwanga.

17. Pamenepo Eli anayankha nati, Pita ndi mtendere; ndipo Mulungu wa Israyeli akupatse copempha cako unacipempha, kwa iye.

18. Ndipo iye anati, Mumkomere mtima mdzakazi wanu. Comweco mkaziyo anamuka, nakadya, ndi nkhope yace siinakhalanso yacisoni.

1 Samueli 1