39. Ndipo Neri anabala Kisi, ndi Kisi anabala Sauli, ndi Sauli anabala Yonatani, ndi Malikisuwa, ndi Abinadabu, ndi Esbaala.
40. Ndipo mwana wa Yonatani ndiye Meribaala; ndi Meribaala anabala Mika.
41. Ndi ana a Mika: Pitoni, ndi Meleki, ndi Tareya, ndi Ahazi.
42. Ndi Ahazi anabala Yara, ndi Yara anabala Ameleti, ndi Azmaveti, ndi Zimri; ndi Zimri anabala Moza,
43. ndi Moza anabala Bineya, ndi Refaya mwana wace, Eleasa mwana wace; Azeli mwana wace;
44. ndi Azeli anali nao ana asanu ndi mmodzi, maina ao ndi awa; Azrikamu, Bokeru, ndi Ismayeli, ndi Seariya, ndi Obadiya, ndi Hanani; awa ndi ana a Azeli.