1 Mbiri 9:1-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Aisrayeli onse anawerengedwa mwa cibadwidwe cao; ndipo taonani, alembedwa m'buku la mafumu a Israyeli; ndipo Yuda anatengedwa ndende kumka ku Babulo cifukwa ca kulakwa kwao.

2. Okhala m'dziko oyamba tsono, akukhala mwao mwao m'roidzi mwao, ndiwo Israyeli, ansembe, Alevi, ndi Anetini.

3. Ndipo m'Yerusalemu munakhala a ana a Yuda, ndi a ana a Benjamini, ndi a ana a Efraimu ndi Manase:

4. Utai mwana wa Amihudi, mwana wa Omri, mwana wa Imri, mwana wa Bani, wa ana a Perezi mwana wa Yuda.

5. Ndipo a Asiloni: Asaya woyamba, ndi ana ace.

6. Ndi a ana a Zera: Yeueli ndi abale ao mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu ndi anai.

7. Ndi a ana a Benjamini: Salu mwana wa Mesulamu, mwana wa Hodavia, mwana wa Hasenuwa;

8. ndi Ibineya mwana wa Yerohamu, ndi Ela mwana wa Uzi, mwana-wa Mikiri, ndi Mesulamu mwana wa Sefatiya, mwana wa Reueli, mwana wa Ibniya,

9. ndi abale ao monga mwa mibadwo yao mazana asanu ndi anai mphambu makumi asanu kudza asanu ndi mmodzi. Onsewa ndiwo akuru a nyumba za makolo ao m'nyumba za makolo ao.

10. Ndi a ansembe: Yedaya, ndi Yehoyaribu, ndi Yakini,

11. ndi Azariya mwana wa Hilikiya, mwana wa Mesulamu, mwana wa Zadoki, mwana wa Merayoti, mwana wa Ahitubu, mtsogoleri wa m'nyumba ya Mulungu;

12. ndi Adaya mwana wa Yerohamu, mwana wa Pasuri, mwana wa Malikiya, ndi Maasai mwana wa Adieli, mwana wa Yazera, mwana wa Mesulamu, mwana wa Mesilemiti, mwana wa Imeri,

13. ndi abale ao, akuru a nyumba za makolo ao cikwi cimodzi mphambu mazana asanu ndi awiri kudza makumi asanu ndi limodzi, anthu odziwitsitsa Debito ya utumiki wa nyumba ya Mulungu.

14. Ndi a Alevi: Semaya mwana wal Hasubu, mwana wa Azrikamu, mwana wa Hasabiya, a ana a Merari;

15. ndi Bakabakara, Heresi, ndi Galala, ndi Mataniya mwana wa Mika, mwana wa Zikiri, mwana wa Asafu;

16. ndi Obadiya mwana wa Semaya, mwana wa Galala, mwana wa Yedutuni, ndi Berekiya mwana wa Asa, mwana wa Elikana, wokhala m'midzi ya Anetofati.

17. Ndi odikira pakhomo: Salumu, ndi Akubu, ndi Talimoni, ndi Ahimani ndi abate ao; Salumu ndi mkuru wao,

18. amene adadikira pa cipata ca mfumu kum'mawa mpaka pomwepo, ndiwo odikira pakhomo a tsasa la ana a Levi.

1 Mbiri 9