1 Mbiri 8:37-40 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

37. ndi Moza anabala Bineya, mwana wace ndiye Rafa, mwana wace Eleasa, mwana wace Azeli;

38. ndipo Azeli anali nao ana asanu ndi mmodzi, maina ao ndiwo Azrikamu, Bokeru, ndi Ismayeli, ndi Seariya, ndi Obadiya, ndi Hanani. Onsewa ndiwo ana a Azeli.

39. Ndi ana a Ezeki mbale wace: Ulamu mwana wace woyamba, Yeusi waciwiri, ndi Elifeleti wacitatu.

40. Ndipo ana a Ulamu ndiwo ngwazi zamphamvu, ndiwo oponya mibvi, nakhala nao ana ambiri ndi zidzukulu zana limodzi. Onsewa ndiwo a ana a Benjamini.

1 Mbiri 8