34. Ndi mwana wa Yonatani ndiye Meri-baala; ndi Meri-baala anabala Mika.
35. Ndi ana a Mika: Pitoni, ndi Meleki, ndi Tareya, ndi Ahazi.
36. Ndi Ahazi anabala Yehoada, ndi Yehoada anabala Alemeti, ndi Azimaveti, ndi Zimri; ndi Zimri anabala Moza;
37. ndi Moza anabala Bineya, mwana wace ndiye Rafa, mwana wace Eleasa, mwana wace Azeli;
38. ndipo Azeli anali nao ana asanu ndi mmodzi, maina ao ndiwo Azrikamu, Bokeru, ndi Ismayeli, ndi Seariya, ndi Obadiya, ndi Hanani. Onsewa ndiwo ana a Azeli.
39. Ndi ana a Ezeki mbale wace: Ulamu mwana wace woyamba, Yeusi waciwiri, ndi Elifeleti wacitatu.
40. Ndipo ana a Ulamu ndiwo ngwazi zamphamvu, ndiwo oponya mibvi, nakhala nao ana ambiri ndi zidzukulu zana limodzi. Onsewa ndiwo a ana a Benjamini.