26. ndi Samserai, ndi Sehariya, ndi Ataliya,
27. ndi Yaaresiya ndi Eliya, ndi Zikiri, ana a Yerohamu.
28. Awa ndi akuru a nyumba za makolo mwa mibadwo yao, ndiwo akuru anakhala m'Yerusalemu awa.
29. Ndipo m'Gibeoni anakhala atate a Gibeoni, dzina la mkazi wace ndiye Maaka;
30. ndi mwana wace woyamba ndiye Abidoni, opondana naye ndi Zuri, ndi Kisi, ndi Baala, ndi Nadabu,
31. ndi Gedoro, ndi Ahiyo, ndi Zekeri.
32. Ndipo Mikiloti anabala Simeya. Ndi iwonso anakhala pamodzi ndi abale ao m'Yerusalemu, popenyana ndi abale ao.
33. Ndipo Neri anabala Kisi, ndi Kisi anabala Sauli, ndi Sauli anabala Yonatani, ndi Malikisuwa, ndi Abinadabu, ndi Esibaala.
34. Ndi mwana wa Yonatani ndiye Meri-baala; ndi Meri-baala anabala Mika.
35. Ndi ana a Mika: Pitoni, ndi Meleki, ndi Tareya, ndi Ahazi.
36. Ndi Ahazi anabala Yehoada, ndi Yehoada anabala Alemeti, ndi Azimaveti, ndi Zimri; ndi Zimri anabala Moza;
37. ndi Moza anabala Bineya, mwana wace ndiye Rafa, mwana wace Eleasa, mwana wace Azeli;
38. ndipo Azeli anali nao ana asanu ndi mmodzi, maina ao ndiwo Azrikamu, Bokeru, ndi Ismayeli, ndi Seariya, ndi Obadiya, ndi Hanani. Onsewa ndiwo ana a Azeli.
39. Ndi ana a Ezeki mbale wace: Ulamu mwana wace woyamba, Yeusi waciwiri, ndi Elifeleti wacitatu.
40. Ndipo ana a Ulamu ndiwo ngwazi zamphamvu, ndiwo oponya mibvi, nakhala nao ana ambiri ndi zidzukulu zana limodzi. Onsewa ndiwo a ana a Benjamini.