1 Mbiri 7:12-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Sufimu yemwe ndi Hupimu ana a Iri, ndi Husimu mwana wa Aheri.

13. Ana a Nafuali: Yazieli, ndi Guni, ndi Yezeri, ndi Salumu, ana a Bila.

14. Ana a Manase ndiwo Asrieli amene mkazi wace anambala, Koma mkazi wace wamng'ono Maramu anabala Makiri atate wa Gileadi;

15. ndi Makiri anadzitengera mkazi, mlongo wace wa Hupimu ndi Supimu, dzina lace ndiye Maaka. Ndipo dzina la mwana waciwiri wa Manase ndiye Tselofekadi. Ndi Tselofekadi anali ndi ana akazi.

16. Ndi Maaka mkazi wa Makiri anabala mwana, namucha dzina lace Peresi, ndi dzina la mbale wace ndiye Seresi, ndi ana ace ndiwo Ulamu, ndi Rakemu.

17. Ndi mwana wa Ulamu: Bedani; ndiwo ana a Gileadi mwana wa Makiri mwana wa Manase.

18. Ndi mlongo wace Hamoleketi anabala Isodi, ndi Abiezeri, ndi Mala.

19. Ndi ana a Semida ndiwo Ahiani, ndi Sekemu, ndi Liki, ndi Aniamu.

20. Ndi ana a Efraimu: Sutera, ndi Beredi mwana wace, ndi Tahati mwana wace, ndi Ekada mwana wace, ndi Tahati mwana wace,

21. ndi Zabadi mwana wace, ndi Sutela mwana wace, ndi Ezeri, ndi Eleadi, amene anthu a Gadi obadwa m'dziko anamupha, popeza anatsikira kukalanda zoweta zao.

22. Ndipo Efraimu atate wao, anacita maliro masiku ambiri, ndi abale ace anadza kudzamtonthoza mtima.

23. Ndipo analowa kwa mkazi wace, naima iye, nabala mwana, namucha dzina lace Beriya, popeza m'nyumba mwace mudaipa.

24. Ndipo mwana wace wamkazi ndiye Seera, amene anamanga Beti-horoni wa kunsi, ndi Beti-horoni wa kumtunda, ndi Uzeniseera.

25. Ndipo Refa anali mwana wace, ndi Resefe, ndi Tela mwana wace, ndi Tahani mwana wace,

1 Mbiri 7