1 Mbiri 6:62-74 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

62. Ndi kwa ana a Gerisomu monga mwa mabanja ao, motapa pa pfuko la Isakara, ndi pa pfuko la Aseri, ndi pa pfuko la Nafitali, ndi pa pfuko la Manase m'Basana, midzi khumi ndi itatu.

63. Ana a Merari analandira mwa maere monga mwa mabanja ao, motapa pa pfuko la Rubeni, ndi pa pfuko la Gadi, ndi pa pfuko la Zebuluni, midzi khumi ndi iwiri.

64. Ndipo ana a Israyeli anapatsa Alevi midzi ndi mabusa ao.

65. Ndipo anapatsa mwamaere, motapa pa pfuko la ana a Yuda, ndi pa pfuko la Simeoni, ndi pa pfuko la ana a Benjamini, midzi iyi yochulidwa maina ao.

66. Ndi mabanja ena a ana a Kohati anali nayo midzi ya malire ao, yotapa pa pfuko la Efraimu.

67. Ndipo anawapatsa midzi yopulumukiramo: Sekemu ndi mabusa ace ku mapiri a Efraimu, Gezeri ndi mabusa ace,

68. ndi Yokimeamu ndi mabusa ace, ndi Betihoroni ndi mabusa ace,

69. ndi Ayaloni ndi mabusa ace, ndi Gatirimoni ndi mabusa ace,

70. ndi motapa pa pfuko la Manase logawika pakati, Aneri ndi mabusa ace, ndi Bileamu ndi mabusa ace, kwa otsala a mabanja a ana a Kohati.

71. Ana a Gerisomu analandira motapa pa mabanja a pfuko la Manase logawika pakati, Golani m'Basana ndi mabusa ace, ndi Asitaroti ndi mabusa ace;

72. ndi motapa pa pfuko la Isakara, Kedesi ndi mabusa ace, Daberati ndi mabusa ace,

73. ndi Ramoti ndi mabusa ace, ndi Anemu ndi mabusa ace;

74. ndi motapa pa pfuko la Aseri, Masala ndi mabusa ace, ndi Abidoni ndi mabusa ace,

1 Mbiri 6