1 Mbiri 4:18-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Ndi mkazi wace Myuda anabala Yeredi atate wa Gedoro, ndi Heberi atate wa Soko, ndi Yekutiyeli atate wa Zanowa. Ndipo awa ndi ana a Bitiya mwana wamkazi wa Farao, amene Meredi anamtenga.

19. Ndi ana a mkazi wa Hodiya, mlongo wace wa Nahamu, ndiwo atate a Kula Mgarimi ndi Esitemowa Mmaaka.

20. Ndi ana a Simoni; Amnoni, ndi Rina, Benehanana, ndi Tiloni. Ndi ana a lsi: Zoheti, ndi Benzoheti.

21. Ana a Sela mwana wa Yuda: Eri atate wa Leka, ndi Laada atate wa Maresa, ndi mabanja a nyumba ya iwo oomba bafuta wa thonje losansitsa a nyumba ya Asibeya,

22. ndi Yokimu, ndi amuna a Kozeba, ndi Yoasi, ndi Sarafa wolamulira m'Moabu, ndi Yasubilehemu; koma mau awa ndiwo a kale lomwe.

23. Iwo ndiwo oumba mbiya, ndi okhala m'Netaimu, ndi m'Gedera; anakhala komweko ndi mfumu m'nchito yace.

24. Ana a Simeoni: Nemueli, ndi Yamini, Yaribi, Zera, Sauli,

25. Salumu mwana wace, Mibsamu mwana wace, Misma mwana wace.

26. Ndi ana a Misma: Hamueli mwana wace, Zakuri mwana wace, Simei mwana wace.

27. Ndipo Simei anali nao ana amuna khumi mphambu asanu ndi mmodzi, ndi ana akazi asanu ndi mmodzi; koma abale ace analibe ana ambiri, ndi banja lao lonse silinacurukitsa ngati ana a Yuda.

28. Ndipo anakhala ku Beereseba, ndi Molada, ndi Hazarasuala,

1 Mbiri 4