1 Mbiri 4:17-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Ndi ana a Ezra: Yeteri, ndi Meredi, ndi Eferi, ndi Yaloni; ndipo anabala Miriamu, ndi Samai, ndi Isba atate wa Esitemowa.

18. Ndi mkazi wace Myuda anabala Yeredi atate wa Gedoro, ndi Heberi atate wa Soko, ndi Yekutiyeli atate wa Zanowa. Ndipo awa ndi ana a Bitiya mwana wamkazi wa Farao, amene Meredi anamtenga.

19. Ndi ana a mkazi wa Hodiya, mlongo wace wa Nahamu, ndiwo atate a Kula Mgarimi ndi Esitemowa Mmaaka.

20. Ndi ana a Simoni; Amnoni, ndi Rina, Benehanana, ndi Tiloni. Ndi ana a lsi: Zoheti, ndi Benzoheti.

21. Ana a Sela mwana wa Yuda: Eri atate wa Leka, ndi Laada atate wa Maresa, ndi mabanja a nyumba ya iwo oomba bafuta wa thonje losansitsa a nyumba ya Asibeya,

22. ndi Yokimu, ndi amuna a Kozeba, ndi Yoasi, ndi Sarafa wolamulira m'Moabu, ndi Yasubilehemu; koma mau awa ndiwo a kale lomwe.

23. Iwo ndiwo oumba mbiya, ndi okhala m'Netaimu, ndi m'Gedera; anakhala komweko ndi mfumu m'nchito yace.

24. Ana a Simeoni: Nemueli, ndi Yamini, Yaribi, Zera, Sauli,

25. Salumu mwana wace, Mibsamu mwana wace, Misma mwana wace.

26. Ndi ana a Misma: Hamueli mwana wace, Zakuri mwana wace, Simei mwana wace.

27. Ndipo Simei anali nao ana amuna khumi mphambu asanu ndi mmodzi, ndi ana akazi asanu ndi mmodzi; koma abale ace analibe ana ambiri, ndi banja lao lonse silinacurukitsa ngati ana a Yuda.

28. Ndipo anakhala ku Beereseba, ndi Molada, ndi Hazarasuala,

29. ndi ku Bila, ndi ku Ezemu, ndi ku Toladi,

30. ndi ku Betueli, ndi ku Horima, ndi ku Zikilaga,

1 Mbiri 4