1. Ana a Yuda: Perezi, Hezroni, ndi Karmi, ndi Huri, ndi Sobala.
2. Ndipo Reaya mwana wa Sobala anabala Yahati; ndi Yahati anabala Ahumai, ndi Lahadi. Iwo ndiwo mabanja a Azorati.
3. Iwo ndiwo a atate wa Etamu: Yezreeli, ndi Isma, ndi Idibasi; ndipo dzina la mlongo wao ndiye Hazeleleponi,
4. ndi Penueli atate wa Gedoro, ndi Ezeri atate wa Husa. Awa ndi ana a Huri woyamba wa Efrata atate wa Betelehemu.
5. Ndipo Asuri atate wa Tekowa anali nao akazi awiri: Hela, ndi Naara.
6. Ndi Naara anambalira Ahuzamu, ndi Heferi, ndi Temeni, ndi Hahastario Iwo ndiwo ana a Naara.
7. Ndi ana a Hela ndiwo Zereti, lzara, ndi Etinani.
8. Ndipo Hakozi anabala Anubu, ndi Zobeba, ndi mabanja a Ahareli mwana wa Harumu.
9. Ndipo Yabezi analemekezedwa koposa abale ace; ndi mace anamucha dzina lace Yabezi, ndi kuti, Popeza ndambala mwaululu.
10. Ndipo Yabezi anaitana kwa Mulungu wa Israyeli, ndi kuti, Mundidalitse ndithu, ndi kukulitsa malire anga; ndi dzanja lanu likhale ndi ine, nimundisunge, kuti coipa cisandibvute. Ndipo Mulungu anafikitsa copempha iye.
11. Ndipo Kelubu mbale wa Sua anabala Mehiri, ndiye atate wa Esitoni.
12. Ndi Esitoni anabala Betirafa, ndi Paseya, ndi Tehina atate wa Irinahasi. Awa ndi anthu a Reka.
13. Ndi ana a Kenazi: Otiniyeli, ndi Seraya; ndi mwana wa Otmiyeh: Hatati.
14. Ndipo Meonotai anabala Ofra; ndi Seraya anabala Yoabu atate wa Geharasimu; popeza iwo ndiwo amisiri.
15. Ndi ana a Kalebi mwana wa Yefune: Iru, Ela, ndi Naamu; ndi ana a Ela, ndi Kenazi.
16. Ndi ana a Yehaleleli: Ziti, ndi Zifa, Tiriya, ndi Asareli.
17. Ndi ana a Ezra: Yeteri, ndi Meredi, ndi Eferi, ndi Yaloni; ndipo anabala Miriamu, ndi Samai, ndi Isba atate wa Esitemowa.
18. Ndi mkazi wace Myuda anabala Yeredi atate wa Gedoro, ndi Heberi atate wa Soko, ndi Yekutiyeli atate wa Zanowa. Ndipo awa ndi ana a Bitiya mwana wamkazi wa Farao, amene Meredi anamtenga.