Ndipo Yabezi anaitana kwa Mulungu wa Israyeli, ndi kuti, Mundidalitse ndithu, ndi kukulitsa malire anga; ndi dzanja lanu likhale ndi ine, nimundisunge, kuti coipa cisandibvute. Ndipo Mulungu anafikitsa copempha iye.