25. Ndipo Yehova anakuza Solomo kwakukuru pamaso pa Aisrayeli onse, nampatsa ulemerero wacifumu, wakuti, asanakhale iyeyu, panalibe mfumu ya Israyeli inali nao wotero.
26. Momwemo Davide mwana wa Jese adakhala mfumu ya Aisrayeli onse.
27. Ndipo nthawi yoti anakhala mfumu ya Israyeli ndiyo zaka makumi anai; zaka zisanu ndi ziwiri anakhala mfumu m'Hebroni, ndi zaka makumi atatu anakhala mfumu m'Yerusalemu.
28. Nafa atakalamba bwino, wocuruka masiku, zolemera, ndi ulemerero; ndi Solomo mwana wace anakhala mfumu m'malo mwaceo