Ndipo taona, pali zigawo za ansembe ndi Alevi, za utumiki wonse wa nyumba ya Mulungu; ndipo pamodzi nawe mu nchito iri yonse pali onse ofuna eni ace aluso, acite za utumiki uli wonse; akuru omwe ndi anthu onse adzacita monga umo udzanenamo.