3. Koma Mulungu anati kwa ine, Sudzamangira dzina langa nyumba, popeza ndiwe munthu wa nkhondo wokhetsa mwazi.
4. Komatu Yehova Mulungu wa Israyeli anasankha ine m'nyumba yonse ya atate wanga, ndikhale mfumu ya Israyeli kosatha; pakuti anasankhiratu Yuda akhale mtsogoleri, ndi m'nyumba ya Yuda nyumba ya atate wanga, ndi mwa ana a atate wanga ndinamkomera ndine, andilonge ufumu wa Israyeli yense;
5. ndi mwa ana anga onse (pakuti Yehova wandipatsa ana amuna ambiri), anasankha Solomo mwana wanga akhale pa mpando wacifumu wa ufumu wa Yehova kuweruza Israyeli.
6. Ndipo anati kwa ine, Solomo mwana wako ndiye adzandimangira nyumba yanga ndi mabwalo anga; pakuti ndamsankha akhale mwana wanga, ndipo Ine ndidzakhala atate wace.
7. Ndipo ndidzakhazikitsa ufumu wace kosatha, akalimbika kucita malamulo anga ndi maweruzo anga monga lero lino.
8. Ndipo tsopano, pamaso pa Aisrayeli onse, khamu la Yehova, ndi m'makutu a Mulungu wathu, sungani, nimufunefune malamulo onse a Yehova Mulungu wanu, kuti mukhale nalo lanu lanu dziko lokoma ili, ndi kulisiyira ana anu pambuyo panu colowa cao kosalekeza.
9. Ndipo iwe Solomo mwana wanga, umdziwe Mulungu wa atate wako, umtumikire ndi mtima wangwiro ndi moyo waufulu; pakuti Yehova asanthula mitima yonse, nazindikira zolingirira zonse za maganizo; ukamfunafuna iye udzampeza, koma ukamsiya iye adzakusiya kosatha.
10. Cenjera tsono, pakuti Yehova anakusankha iwe umange nyumba ya malo opatulika; limbika, nucite.
11. Pamenepo Davide anapatsa Solomo mwana wace cifaniziro ca likole la kacisi, ndi ca nyumba zace, ndi ca zosungiramo cuma zace, ndi ca zipinda zosanjikizana zace, ndi ca zipinda zace za m'katimo, ndi ca kacisi wotetezerapo;
12. ndi cifaniziro ca zonse anali nazo mwa mzimu, ca mabwalo a nyumba ya Yehova, ndi ca zipinda zonse pozungulirapo, ca zosungiramo cuma za nyumba ya Mulungu, ndi ca zosungiramo cuma za zinthu zopatulika;
13. ndi ca magawidwe a ansembe ndi Alevi, ndi ca nchito zonse za utumiki wa nyumba ya Yehova, ndi ca zipangizo za utumiki wa nyumba ya Yehova;
14. ca golidi woyesedwa kulemera kwace wa zipangizo zagolidi, wa zipangizo zonse za nchito ya mtundu uli wonse; ca siliva wa zipangizo zasiliva woyesedwa kulemera kwace, wa zipangizo za nchito ya mitundu mitundu;
15. mwa kulemera kwacenso ca zoikapo nyali zagolidi, ndi nyali zace zagolidi, mwa kulemera kwace ca coikapo nyali ciri conse, ndi nyali zace; ndi ca zoikapo nyali zasiliva, siliva woyesedwa kulemera kwace wa coikapo nyali ciri conse, ndi nyali zace, monga mwa coikapo nyali ciri conse;
16. ndi golidi woyesedwa kulemera kwace wa magome a makate woonekera, wa gome liri lonse; ndi siliva wa magome asiliva,
17. ndi mitengo, ndi mbale zowazira, ndi zikho za golidi woona, ndi ca mitsuko yace yagolidi, woyesedwa kulemera kwace mtsuko uli wonse; ndi ca mitsuko yasiliva woyesedwa kulemera kwace mtsuko uli wonse;
18. ndi ca guwa la nsembe lofukizapo la golidi woyengetsa woyesedwa kulemera kwace, ndi cifaniziro ca gareta wa akerubi agolidi akufunyulula mapiko ao ndi kuphimba likasa la cipangano la Yehova.