12. Wacisanu ndi cinai wa mwezi wacisanu ndi cinai ndiye Abiezeri M-anatoti wa Abenjamini; ndi m'cigawo mwace zikwi makumi awiri mphambu zinai.
13. Wakhumi wa mwezi wakhumi ndiye Maharai Mnetofati wa Azera; ndi m'cigawo mwace zikwi makumi awiri mphambu zinai.
14. Wakhumi ndi cimodzi wa mwezi wakhumi ndi cimodzi ndiye Benaya Mpiratoni wa ana a Efraimu; ndi m'cigawo mwace zikwi makumi awiri mphambu zinai.
15. Wakhumi ndi ciwiri wa mwezi wakhumi ndi ciwiri ndiye Heledai Mnetofati wa Otiniyeli; ndi m'cigawo mwace zikwi makumi awiri mphambu zinai.
16. Koma oyang'anira mafuko a lsrayeli ndi awa: wa Arubeni mtsogoleri wao ndiye Eliezeri mwana wa Zikiri; wa Asimeoni, Sefatiya mwana wa Maaka;
17. wa Alevi, Hasabiya mwana wa Kemueli; wa Aroni, Zadoki;
18. wa Yuda, Elihu mbale wina wa Davide; wa Isakara, Omri mwana wa Mikaeli;
19. wa Zebuluni, Isimaya mwana wa Obadiya; wa Nafitali, Yeremoti mwana wa Azrieli;
20. wa ana a Efraimu, Hoseya mwana wa Azaziya; wa pfuko la Manase logawika pakati, Yoeli mwana wa Pedaya;
21. wa pfuko la Manase logawika pakati m'Gileadi, Ido mwana wa Zekariya; wa Benjamini, Yasiyeli mwana wa Abineri;
22. wa Dani, Azareli mwana wa Yerohamu. Awa ndi akazembe a mapfuko a Israyeli.
23. Koma Davide sanawerenga iwo a zaka makumi awiri ndi ocepapo, pakuti Yehova adati kuti adzacurukitsa Israyeli ngati nyenyezi za kuthambo.
24. Yoabu mwana wa Zeruya anayamba kuwerenga, koma sanatsiriza; ndi mkwiyo unagwera Israyeli cifukwa ca ici, ndipo ciwerengo cao sicinalembedwa m'buku la mbiri ya mfumu Davide.
25. Ndipo woyang'anira cuma ca mfumu ndiye Azimaveti mwana wa Adiyeli, ndi woyang'anira wa cuma ca m'minda, m'mizinda ndi m'miraga, ndi nyumba za nsanja, ndiye Yonatani mwana wa Uziya;
26. ndi woyang'anira iwo akugwira nchito ya m'munda yakulima nthaka ndiye Ezri mwana wa Kelubi;