1 Mbiri 23:22-32 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

22. Nafa Eleazara wopanda ana amuna, koma ana akazi ndiwo; ndi asuweni ao ana a Kisi anawatenga akhale akazi ao.

23. Ana a Musi: Mali, ndi Ederi, ndi Yeremoti; atatu.

24. Awa ndi ana a Levi monga mwa nyumba za makolo ao, ndiwo akuru a nyumba za makolo a iwo owerengedwa mwa ciwerengo ca maina mmodzi mmodzi, akugwira nchito ya utumiki wa nyumba ya Yehova, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu.

25. Pakuti Davide anati, Yehova Mulungu wa Israyeli wapumulitsa anthu ace; ndipo akhala m'Yerusalemu kosatha;

26. ndiponso Alevi asasenzenso kacisi ndi zipangizo zace zonse za utumiki wace.

27. Pakuti monga mwa mau ace otsiriza a Davide, ana a Levi anawerengedwa kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu.

28. Pakuti nchito yao ndiyo kuimirira ana a Aroni, atumikire m'nyumba ya Yehova, m'mabwalo, ndi kuzipinda, ndi kuyeretsa zopatulika zonse; inde nchito za utumiki wa nyumba ya Mulungu;

29. ya mkate woonekera womwe, ndi ya ufa wosalala wa nsembe yaufa, ndi ya timitanda taphanthiphanthi topanda cotupitsa, ndi ya ciwaya, ndi yakukazinga, ndi ya miyeso iri yonse;

30. ndi kuimirira m'mawa ndi m'mawa kuyamika ndi kulemekeza Yehova, momwemonso madzulo;

31. ndi kupereka nsembe zopsereza zonse kwa Yehova, za masabata, za pokhala mwezi, za nyengo zoikika, kuwerenga kwace monga mwa lemba lace, kosalekeza pamaso pa Yehova;

32. ndi kuti asunge udikiro wa cihema cokomanako, ndi udikiro wa malo opatulika ndi udikiro wa ana a Aroni abale ao, potumikira nyumba ya Yehova.

1 Mbiri 23