1 Mbiri 21:4-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Koma mau a mfumu anamlaka Yoabu. Naturuka Yoabu, nakayendayenda mwa Aisrayeli onse, nadza ku Yerusalemu.

5. Ndipo Yoabu anapereka kwa Davide ciwerengo ca anthu owerengedwa. Ndipo Aisrayeli onse anali zikwi mazana khumi ndi limodzi osolola lupanga, ndi Yuda anali zikwi mazana anai mphambu makumi asanu ndi awiri akusolola lupanga,

6. Koma sanawerenga Alevi ndi Abenjamini pakati pao; pakuti mau a mfumu anamnyansira Yoabu.

7. Ndipo Mulungu anaipidwa naco cinthuci, cifukwa cace iye anakantha Israyeli.

1 Mbiri 21