16. Ndipo Davide anakweza maso ace, naona mthenga wa Yehova alikuima pakati pa dziko ndi thambo, ali nalo lupanga losolola m'dzanja lace, lotambasukira pa Yerusalemu. Pamenepo Davide ndi akuru obvala ziguduli anagwa nkhope zao pansi.
17. Ndipo Davide anati kwa Mulungu, Si ndine nanga ndalamulira kuti awerenge anthu? Inde, ndine amene ndacimwa ndi kucita coipa ndithu; koma nkhosa izi zinacitanji? dzanja lanu, Yehova Mulungu wanga, Gnditsutse ine ndi nyumba ya atate wanga, koma Gsatsutse anthu anu ndi kuwacitira mliri.
18. Pamenepo mthenga wa Yehova anauza Gadi kuti anene ndi Davide, akwere Davideyo kuutsira Yehova guwa la nsembe pa dwale la Orinani Myebusi,
19. Ndipo Davide anakwera monga mwa mau a Gadi adawanena m'dzina la Yehova.
20. Poceuka Orinani anaona wamthengayo; ndi ana ace amuna anai anali naye anabisala. Koma Orinani analikupuntha tirigu.
21. Ndipo pofika Davide kwa Orinani, Orinaniyo anapenyetsa, naona Davide, naturuka kudwale, nawerama kwa Davide, nkhope yace pansi.
22. Davide tsono anati kwa Orinani, Ndipatse padwale pano kuti ndimangepo guwa la nsembe la Yehova; undipatse gi pa mtengo wace wonse, kuti mliri ulekeke pa anthu.
23. Ndipo Orinani anati kwa Davide, Mulitenge, ndi mbuye wanga mfumu icite comkomera m'maso mwace; taonani, ndikupatsani ng'ombe za nsembe zopsereza; ndi zipangizo zopunthira zikhale nkhuni, ndi tirigu wa nsembe yaufa; ndizipereka zonse.
24. Koma mfumu Davide anati kwa Orinani, lai, koma ndidzaligula pa mtengo wace wonse; pakuti sindidzatengera Yehova ciri cako, kapena kupereka nsembe yopsereza yopanda mtengo wace.
25. Momwemo Davide anapatsa Orinani cogulira malowa golidi wa masekeli mazana asanu ndi limodzi kulemera kwace.
26. Ndipo Davide anamangira Yehova guwa la nsembe komweko; napereka nsembe zopsereza, ndi nsembe zoyamika, naitana kwa Yehova; ndipo anamyankha ali m'Mwamba ndi mota pa guwa la nsembe yopsereza.
27. Ndipo Yehova anauza wamthenga kuti abweze lupanga lace m'cimace.
28. Nthawi yomweyi, pakuona Davide kuti Yehova anambvomereza pa dwale la Orinani Myebusi, anaphera nsembe pomwepo.
29. Pakuti kacisi wa Yehova amene Mose anapanga m'cipululu, ndi guwa la nsembe yopsereza, zinali pa msanje wa ku Gibeoni nthawi yomweyi.
30. Kama Davide sanathe kumuka kukhomo kwace kufunsira kwa Mulungu, pakuti anaopa lupanga la mthenga wa Yehova.