1 Mbiri 21:11-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Nadza Gadi kwa Davide, nanena naye, Atero Yehova, Dzitengereko;

12. kapena zaka zitatu za njala; kapena miyezi itatu ya kuthedwa pamaso pa adani ako, ndi kuti lupanga la adani ako likupeze; kapena masiku atatu lupanga la Yehova, ndilo mliri m'dzikomo, ndi mthenga wakuononga wa Yehova mwa malire onse a Israyeli, Ulingirire tsono, ndimbwezere mau anji iye amene anandituma ine?

13. Ndipo Davide anati kwa Gadi, Ndipsinjika kwambiri; ndigwere m'dzanja la Yehova, pakuti zifundo zace zicurukadi; koma ndisagwere m'dzanja la munthu.

14. Momwemo Yehova anatumiza mliri pa Israyeli; ndipo adagwapo amuna zikwi makumi asanu ndi awiri a Israyeli.

15. Ndipo Mulungu anatuma mthenga ku Yerusalemu kuuononga; ndipo poti auononge, Yehova anapenya, naleka coipaci; nati kwa mthenga wakuononga, Cakwanira, bweza dzanja lako tsopano. Ndi mthenga wa Yehova anaima pa dwale la Orinani Myebusi,

1 Mbiri 21