5. Pamenepo anamuka ena, namuuza Davide za amunawa. Natumiza iye kukomana nao, pakuti amunawa anacita manyazi kwambiri. Ndipo mfumu inati, Balindani ku Yeriko mpaka zamera ndebvu zanu; zitamera mubwere.
6. Ndipo pamene ana a Amoni anaona kuti anadzinunkhitsa kwa Davide, Hanuni ndi ana a Amoni anatumiza matalente cikwi cimodzi a siliva, kudzilembera magareta ndi apakavalo ku Mesopotamiya, ndi ku Aramu-maaka, ndi ku Zoba.
7. Momwemo anadzilembera magareta zikwi makumi atatu mphambu ziwiri, ndi mfumu ya Maaka ndi anthu ace; nadza iwo, namanga misasa cakuno ca Medeba. Ana a Amoni omwe anasonkhana m'midzi mwao, nadza kunkhondo.
8. Pamene Davide anamva ici anatuma Yoabu ndi gulu lonse la anthu amphamvu.
9. Ndipo ana a Amoni anaturuka, nandandalitsa nkhondo ku cipata ca mudzi, ndi mafumu adadzawo anali pa okha kuthengo.
10. Pakuona Yoabu tsono kuti nkhondo inamdzera kumaso ndi kumbuyo, anasankha amuna osankhika onse a Israyeli, nawanika ayambane ndi Aaramu.
11. Ndipo anthu otsala anawapereka m'dzanja la Abisai mbale wace; ndipo anadzinika avambane ndi ana a Amoni.
12. Ndipo anati, Akandilaka Aaramu, udzandilanditsa ndiwe; koma akakulaka ana a Amoni, ndidzakulanditsa ndine.
13. Limbika mtima, tilimbikire anthu athu, ndi midzi ya Mulungu wathu; ndipo Yehova acite comkomera.
14. Pamenepo Yoabu ndi anthu anali naye anayandikira pamaso pa Aaramu kulimbana nao, ndipo anawathawa.