11. Izi zomwe mfumu Davide anazipatulira Yehova, pamodzi ndi siliva ndi golidi adazitenga kwa amitundu onse, kwa Edomu, ndi kwa Moabu, ndi kwa ana a Amoni, ndi kwa Afilisti, ndi kwa Amaleki.
12. Ndipo Abisai mwana wa Zeruya anakantha Aedomu m'Cigwa ca Mcere zikwi khumi mphambu zisanu ndi zitatu.
13. Ndipo anaika asilikari a boma m'Edomu; ndi Aedomu onse anasanduka anthu a Davide. Ndipo Yehova anasunga Davide kuli konse anamukako.
14. Ndipo Davide anakhala mfumu ya Aisrayeli onse, naweruza anthu ace onse, nawacitira cilungamo.