1 Mbiri 17:8-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. ndipo ndakhala ndi iwe kuli konse unamukako, ndi kuononga adani ako onse pamaso pako; ndipo ndakubukitsira dzina lakunga dzina la akuru okhala padziko.

9. Ndipo ndaikira anthu anga Israyeli malo, ndi kuwaoka, kuti akhale m'malo mwao osasunthikanso; ndi ana osalungama sadzawapululanso monga poyamba paja;

10. ndi kuyambira kuja ndinaika oweruza ayang'anire anthu anga Israyeli; ndipo ndagonjetsa adani ako onse. Ndikuuzanso kuti Yehova adzakumangira banja.

11. Ndipo kudzacitika, atakwanira masiku ako kuti uzipita kukhala ndi makolo ako, ndidzaukitsa mbeu yako pambuyo pako, ndiye wa ana ako; ndipo ndidzakhazikitsa ufumu wace.

12. Iye adzandimangira nyumba; ndipo ndidzakhazikitsa mpando wacifumu wace kosatha.

13. Ndidzakhala atate wace, ndi iye adzakhala mwana wanga; ndipo sindidzamcotsera cifundo canga monga muja ndinacotsera iye amene anakhala usanakhale iwe;

14. koma ndidzamkhazikitsa m'nyumba mwanga, ndi m'ufumu wanga kosatha; ndi mpando wa cifumu wace udzakhazikika kosatha.

15. Monga mwa mau awa onse, ndi monga mwa masomphenya awa onse, momwemo Natani analankhula ndi Davide.

16. Pamenepo mfumu Davide analowa nakhala pamaso pa Yehova, nati, Ndine yani, Yehova Mulungu, ndi nyumba yanga njotani kuti mwandifikitsa mpaka pano?

17. Ndipo ici ncacing'ono pamaso panu, Mulungu, koma mwanena za nyumba ya mtumiki wanu nthawi yam'tsogolo ndithu, ndipo mwandiyesera ngati munthu womveka, Yehova Mulungu.

18. Anenenjinso Davide kwa Inu za ulemu wocitikira mtumiki wanu? pakuti mudziwa mtumiki wanu.

19. Yehova, cifukwa ca mtumiki wanu, ndi monga mwa mtima wanu, mwacita ukulu uwu wonse, kundidziwitsa zazikuru izi zonse.

20. Yehova, palibe wina wonga inu, palibenso Mulungu wina koma Inu; monga mwa zonse tazimva m'makutu mwathu.

21. Ndiwo ayani akunga anthu anu Israyeli, mtundu wa pa wokha wa pa dziko lapansi, amene Mulungu anakadziombolera mtundu wa anthu, kudzibukitsira dzina, mwa zazikuru ndi zoopsa, pakupitikitsa amitundu pamaso pa anthu anu amene munawaombola m'Aigupto?

22. Pakuti anthu anu Israyeli mudawayesa anthu anu anu kosatha; ndipo Inu, Yehova, munayamba kukhala Mulungu wao.

1 Mbiri 17