1 Mbiri 17:7-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Cifukwa cace tsono, uzitero naye mtumiki wanga Davide, Atero Ambuye wa makamu, Ndinakutenga kubusa potsata iwe nkhosa, kuti ukhale mtsogoleri wa anthu anga Israyeli;

8. ndipo ndakhala ndi iwe kuli konse unamukako, ndi kuononga adani ako onse pamaso pako; ndipo ndakubukitsira dzina lakunga dzina la akuru okhala padziko.

9. Ndipo ndaikira anthu anga Israyeli malo, ndi kuwaoka, kuti akhale m'malo mwao osasunthikanso; ndi ana osalungama sadzawapululanso monga poyamba paja;

10. ndi kuyambira kuja ndinaika oweruza ayang'anire anthu anga Israyeli; ndipo ndagonjetsa adani ako onse. Ndikuuzanso kuti Yehova adzakumangira banja.

11. Ndipo kudzacitika, atakwanira masiku ako kuti uzipita kukhala ndi makolo ako, ndidzaukitsa mbeu yako pambuyo pako, ndiye wa ana ako; ndipo ndidzakhazikitsa ufumu wace.

1 Mbiri 17