1 Mbiri 16:7-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Tsiku limenelo tsono Davide anayamba kuwapatsa nyimbo ya kuyamika nayo Yehova; ocita ndiwo Asafu ndi abale ace.

8. Yamikani Yehova, itanani dzina lace;Bukitsani mwa mitundu ya anthu zocita iye.

9. Myimbireni, myimbireni zomlemekeza;Fotokozerani zodabwiza zace zonse.

10. Mudzitamandire ndi dzina lace lopatulika;Mitima yao ya iwo ofuna Yehova ikondwere.

1 Mbiri 16