5. Asafu ndiye mkuru wao, ndi otsatana naye Zekariya, Yeieli, ndi Semiramoti, ndi Yehieli, ndi Matitiya, ndi Eliabu, ndi Benaya, ndi Obedi Edomu, ndi Yeieli, ndi zisakasa ndi azeze; koma Asafu ndi nsanje zomvekatu;
6. ndi Benaya ndi Yahazieli ansembe ndi malipenga kosalekeza, ku likasa la cipangano la Mulungu.
7. Tsiku limenelo tsono Davide anayamba kuwapatsa nyimbo ya kuyamika nayo Yehova; ocita ndiwo Asafu ndi abale ace.
8. Yamikani Yehova, itanani dzina lace;Bukitsani mwa mitundu ya anthu zocita iye.
9. Myimbireni, myimbireni zomlemekeza;Fotokozerani zodabwiza zace zonse.
10. Mudzitamandire ndi dzina lace lopatulika;Mitima yao ya iwo ofuna Yehova ikondwere.
11. Funsirani kwa Yehova ndi mphamvu yace;Funani nkhope yace nthawi zonse.
12. Kumbukilani zodabwiza zace adazicita,Zizindikilo zace, ndi maweruzo a pakamwa pace;
13. Inu mbeu ya Israyeli mtumiki wace,Inu ana a Yakobo, osankhika ace.
14. Iye ndiye Yehova Mulungu wathu;Maweruzo ace akhala pa dziko lonse lapansi,
15. Kumbukilani cipangano cace kosatha,Mauwo anawalamulira mibadwo zikwi;