15. Kumbukilani cipangano cace kosatha,Mauwo anawalamulira mibadwo zikwi;
16. Cipanganoco anapangana ndi Abrahamu,Ndi lumbiro lace ndi Isake;
17. Ndipo anacitsimikizirakwa Yakobo cikhale malemba,Cikhale cipangano cosatha kwa Israyeli;
18. Ndi kunena kuti, Ndidzakupatsa iwe dziko la Kanani,Gawo la colandira cako;
19. Pokhala inu anthu owerengeka,Inde anthu pang'ono, ndi alendo m'mwemo;
20. Nayendayenda kucokera mtundu wina kufikira mtundu wina,Kucokera ufumu wina kufikira anthu ena.
21. Sanalola munthu awasautse;Ndipo anadzudzula mafumu cifukwa ca iwowa;