1 Mbiri 16:1-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo analowa nalo likasa la Mulungu, nalgka pakati pa hemalo Davide adaliutsira; ndipo anapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zoyamika pamaso pa Mulungu.

2. Ndipo atatha Davide kupereka nsembe zopsereza ndi nsembe zoyamika, anadalitsa anthu m'dzina la Yehova.

3. Nagwira ali yense wa Israyeli, wamwamuna ndi wamkazi, yense mtanda wa mkate, ndi nthuli ya nyama, ndi ncinci ya mphesa zouma.

4. Ndipo anaika Alevi ena atumikire ku likasa la Yehova, nalalikire, nayamike, nalemekeze Yehova Mulungu wa Israyeli.

5. Asafu ndiye mkuru wao, ndi otsatana naye Zekariya, Yeieli, ndi Semiramoti, ndi Yehieli, ndi Matitiya, ndi Eliabu, ndi Benaya, ndi Obedi Edomu, ndi Yeieli, ndi zisakasa ndi azeze; koma Asafu ndi nsanje zomvekatu;

6. ndi Benaya ndi Yahazieli ansembe ndi malipenga kosalekeza, ku likasa la cipangano la Mulungu.

7. Tsiku limenelo tsono Davide anayamba kuwapatsa nyimbo ya kuyamika nayo Yehova; ocita ndiwo Asafu ndi abale ace.

8. Yamikani Yehova, itanani dzina lace;Bukitsani mwa mitundu ya anthu zocita iye.

9. Myimbireni, myimbireni zomlemekeza;Fotokozerani zodabwiza zace zonse.

10. Mudzitamandire ndi dzina lace lopatulika;Mitima yao ya iwo ofuna Yehova ikondwere.

11. Funsirani kwa Yehova ndi mphamvu yace;Funani nkhope yace nthawi zonse.

12. Kumbukilani zodabwiza zace adazicita,Zizindikilo zace, ndi maweruzo a pakamwa pace;

13. Inu mbeu ya Israyeli mtumiki wace,Inu ana a Yakobo, osankhika ace.

14. Iye ndiye Yehova Mulungu wathu;Maweruzo ace akhala pa dziko lonse lapansi,

15. Kumbukilani cipangano cace kosatha,Mauwo anawalamulira mibadwo zikwi;

1 Mbiri 16