1 Mbiri 14:12-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Ndipo anasiyako milungu yao; nalamula Davide, ndipo anaitentha ndi moto.

13. Ndipo Afilisti anabwerezanso, nafalikira m'cigwamo.

14. Ndipo Davide anafunsiranso kwa Mulungu, nanena Mulungu naye, Usakwera kuwatsata, uwazungulire, nuwadzere pandunji pa mitengo ya mkandankhuku.

15. Ndipo kudzali, pakumva iwe kuwayula kunsonga kwa mitengo ya mkandankhuku, pamenepo uturukire kunkhondo; pakuti Mulungu waturukira pamaso pako kukantha gulu la Afilisti.

1 Mbiri 14