20. Pomuka iye ku Zikilaga anapambukira kwa iye a Manase: Adina, ndi Yozabadi, ndi Yedyaeli, ndi Mikaeli, ndi Yozabadi, ndi Elihu, ndi Ziletai, akuru a zikwi a ku Manase.
21. Ndipo anathandiza Davide aponyane nalo gulu la acifwamba, pakuti onse ndiwo ngwazi zamphamvu, nakhala atsogoleri m'khamu la nkhondo.
22. Pakuti nthawi yomweyo anadza kwa Davide kumthandiza, mpaka kunali nkhondo yaikuru; ngati nkhondo ya Mulungu.
23. Ndipo kuwerenga kwa akuru okonzekeratu kunkhondo, anadzawo kwa Davide ku Hebroni, kupambukitsa ufumu wa Sauli ukhale wace, monga mwa mau a Yehova, ndi: uku.
24. Ana a Yuda akunyamula zikopa ndi mikondo ndiwo zikwi zisanu ndi cimodzi mphambu mazana asanu ndi atatu, okonzekeratu kunkhondo.
25. A ana a Simeoni ngwazi zamphamvu za nkhondo zikwi zisanu ndi ziwiri mphambu zana liimodzi.
26. A ana a Levi zikwi zinai mphambu mazana asanu ndi limodzi.
27. Ndipo Yehoyada, ndiye mtsogoleri wa Aaroni, ndi pamodzi nave zikwi zitatu mphambu mazana asanu ndi awiri;
28. ndi Zadoki, ndiye mnyamata, ngwazi yamphamvu, ndi a nyumba ya kholo lace, akuru makumi awiri mphambu awfri.
29. Ndi a ana a Benjamini, abale a Sauli, zikwi zitatu; pakuti mpaka pomwepo ocuruka a iwowa anaumirira nyumba ya Sauli.
30. Ndi a ana a Efraimu zikwi makumi awiri mphambu mazana asanu ndi atatu, ngwazi zamphamvu, anthu omveka m'nyumba za makolo ao.
31. Ndipo a pfuko la Manase logawika pakati zikwi khumi mphambu zisanu ndi zitatu, ochulidwa maina ao kuti adzalonge Davide mfumu.