20. Pomuka iye ku Zikilaga anapambukira kwa iye a Manase: Adina, ndi Yozabadi, ndi Yedyaeli, ndi Mikaeli, ndi Yozabadi, ndi Elihu, ndi Ziletai, akuru a zikwi a ku Manase.
21. Ndipo anathandiza Davide aponyane nalo gulu la acifwamba, pakuti onse ndiwo ngwazi zamphamvu, nakhala atsogoleri m'khamu la nkhondo.
22. Pakuti nthawi yomweyo anadza kwa Davide kumthandiza, mpaka kunali nkhondo yaikuru; ngati nkhondo ya Mulungu.
23. Ndipo kuwerenga kwa akuru okonzekeratu kunkhondo, anadzawo kwa Davide ku Hebroni, kupambukitsa ufumu wa Sauli ukhale wace, monga mwa mau a Yehova, ndi: uku.
24. Ana a Yuda akunyamula zikopa ndi mikondo ndiwo zikwi zisanu ndi cimodzi mphambu mazana asanu ndi atatu, okonzekeratu kunkhondo.