1 Mbiri 12:19-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Ena a Manase omwe anapambukira kwa Davide, muja iye anadza ndi Afilisti koponyana nkhondo ndi Sauli, koma sanawathandiza; popeza akalonga a Afilisti, atacita upo, anamuuza acoke, ndi kuti, Adzapambukira kwa mbuye wace Sauli ndi kutisandulikira.

20. Pomuka iye ku Zikilaga anapambukira kwa iye a Manase: Adina, ndi Yozabadi, ndi Yedyaeli, ndi Mikaeli, ndi Yozabadi, ndi Elihu, ndi Ziletai, akuru a zikwi a ku Manase.

21. Ndipo anathandiza Davide aponyane nalo gulu la acifwamba, pakuti onse ndiwo ngwazi zamphamvu, nakhala atsogoleri m'khamu la nkhondo.

22. Pakuti nthawi yomweyo anadza kwa Davide kumthandiza, mpaka kunali nkhondo yaikuru; ngati nkhondo ya Mulungu.

23. Ndipo kuwerenga kwa akuru okonzekeratu kunkhondo, anadzawo kwa Davide ku Hebroni, kupambukitsa ufumu wa Sauli ukhale wace, monga mwa mau a Yehova, ndi: uku.

24. Ana a Yuda akunyamula zikopa ndi mikondo ndiwo zikwi zisanu ndi cimodzi mphambu mazana asanu ndi atatu, okonzekeratu kunkhondo.

25. A ana a Simeoni ngwazi zamphamvu za nkhondo zikwi zisanu ndi ziwiri mphambu zana liimodzi.

26. A ana a Levi zikwi zinai mphambu mazana asanu ndi limodzi.

1 Mbiri 12