1. Ndipo kunacitika zitapita zaka mazana anai mphambu makumi asanu ndi atatu ataturuka ana a Israyeli m'dziko la Aigupto, caka cacinai cakukhala Solomo mfumu ya Israyeli, m'mwezi wa Zivi, ndiwo mwezi waciwiri, iye anayamba kumanga nyumba ya Yehova.
2. Ndipo nyumbayo mfumu Solomo anaimangira Yehova, m'litali mwace munali mikono makumi asanu ndi limodzi, ndi m'mimba mwace mikono makumi awiri, ndi msinkhu wace mikono makumi atatu.
3. Ndipo anamanga likole pakhomo pa nyumba ya kacisiyo, m'litali mwace munali mikono makumi awiri monga m'mimba mwace mwa nyumbayo, kupingasa kwace kunali mikono khumi ku khomo la nyumba.
4. Ndipo m'nvumbamo anamanga mazenera a made okhazikika.
5. Ndipo anamanga zipinda zosanjikizana zogundana ndi khoma, kuzungulira makoma a nyumba ya Kacisi, ndi monenera momwemo; namanga zipinda zozinga,
6. Cipinda capansico kupingasa kwace kunali mikono isanu, capakatico kupingasa kwace mikono isanu ndi umodzi, cacitatuco kupingasa kwace mikono isanu ndi iwiri; pakuti kubwalo anacepsa khoma pozungulirapo, mitanda isalongedwe m'makoma a nyumba.
7. Ndipo nyumbayo pomangidwa inamangidwa ndi miyala yokonzeratu asanaitute; ndipo m'nyumbamo simunamveka: kulira nyundo, kapena nkhwangwa, kapena cipangizo cacitsulo, pomangidwa iyo.