4. Pakutinso, pamenetinali ndi inu tinakuuziranitu kuti tidzamva zisautso; monga kudacitika, monganso mudziwa.
5. Mwa ici inenso, posalekereranso, ndinatuma kukazindikira cikhulupiriro canu, kuti kaperta: woyesa akadakuyesani, ndipo cibvuto cathu cikadakhala copanda pace.
6. Koma tsopano pofika Timoteo kwathu kucokera kwa inu, ndi kutifotokozera mbiri yokoma ya cikhulupiriro ndi cikondano canu, ndi kuti mutikumbukila bwino masiku onse, pokhumba kutiona ife, monganso ire kukuonani inu;
7. cifukwa ca ici tasangalala pa inu, abale, m'kupsinjika kwathu konse ndi cisautso cathu conse, mwa cikhulupiriro canu;
8. pakuti tsopano tiri ndi moyo, ngati inu mucirimika mwa Ambuye.
9. Pakuti tikhoza kubwezera kwa Mulungu ciyamiko canji cifukwa ca inu, pa cimwemwe conse tikondwera naco mwa inu pamaso pa Mulungu wathu;
10. ndi kucurukitsa mapemphero athu usiku ndi usana kuti tikaone nkhope yanu, ndi kukwaniritsa zoperewera pa cikhulupiriro canu?