1 Atesalonika 3:10-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. ndi kucurukitsa mapemphero athu usiku ndi usana kuti tikaone nkhope yanu, ndi kukwaniritsa zoperewera pa cikhulupiriro canu?

11. Koma Mulungu Atate wathu mwini yekha, ndi Ambuye wathu Yesu atitsogolere m'njira yakufika kwa inu;

12. koma Ambuye akukulitseni inu, nakueurukitseni m'cikondano wina kwa mnzace ndi kwa anthu onse, monganso ife titero kwa inu;

13. kuti akakhazikitse mitima yanu yopanda cifukwa m'ciyero pamaso pa Mulungu Atate wathu, pakufika Ambuye wathu Yesu pamodzi ndi oyera mtima ace onse.

1 Atesalonika 3