4. Ndiponso ndiri ndi ciani ndi inu, Turo ndi Zidoni, ndi malire onse a Afilisti? mudzandibwezera cilango kodi? Mukandibwezera cilango msanga, mofulumira, ndidzabwezera cilango canu pamutu panu,
5. Popeza inu munatenga siliva wanga ndi golidi wanga, ndi kulonga zofunika zanga zokoma m'akacisi anu;
6. munagulitsanso ana a Yuda ndi ana a Yerusalemu kwa ana a Yavani, kuwacotsa kutali kwa malire ao;
7. taonani, ndidzawautsa kumalo kumene munawagulitsako, ndi kubwezera cilango canu pamutu panu;
8. ndipo ndidzagulitsa ana ako amuna ndi akazi m'dzanja la ana a Yuda; ndipo iwo adzawagulitsa kwa anthu a Seba, kwa anthu okhala kutari; pakuti Yehova wanena.
9. Mulalikire ici mwa amitundu mukonzeretu nkhondo; utsani amuna amphamvu; amuna onse a nkhondo ayandikire nakwere.
10. Sulani makasu anu akhale malupanga, ndi anangwape anu akhale nthungo; wofoka anene, Ndine wamphamvu.
11. Fulumirani, idzani, amitundu inu nonse pozungulirapo; sonkhanani pamodzi, mutsitsire komweko amphamvu anu, Yehova.
12. Agalamuke amitundu, nakwerere ku cigwa ca Yosafati; pakuti ndidzakhala komweko kuweruza amitundu onse ozungulira,