Yoweli 3:17-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Momwemo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu wakukhala m'Ziyoni, phiri langa lopatulika; pamenepo Yerusalemu adzakhala wopatulika, osapitanso alendo pakati pace,

18. Ndipo kudzacitika tsiku ilo mapiri adzakhetsa vinyo wozuna, ndi pazitunda padzayenda mkaka, ndi m'mitsinje yonse ya Yuda mudzayenda madzi; ndi madzi a kasupe adzaturuka m'nyumba ya Yehova, nadzamwetsa madzi cigwa ca Sitimu.

19. Aigupto adzasanduka bwinja, ndi Edomu adzasanduka cipululu copanda kanthu, cifukwa ca ciwawaci anawacitira ana a Yuda; popeza anakhetsa mwazi wosacimwa m'dziko lao.

20. Koma Yuda adzakhala cikhalire, ndi Yerusalemu ku mibadwo mibadwo.

21. Ndipo ndidzayeretsa mwazi wao umene sindinauyeretsa, pakuti Yehova akhala m'Ziyoni.

Yoweli 3