4. Maonekedwe ao aoneka ngati akavalo, nathamanga ngati akavalo a nkhondo.
5. Atumphako ngati mkokomo wa magareta pamwamba pa mapiri, ngati kulilima kwa malawi a moto akupsereza ziputu, ngati mtundu wamphamvu wa anthu ondandalikira nkhondo.
6. Pamaso pao mitundu ya anthu ikumva zowawa, nkhope zonse zitumbuluka.
7. Athamanga ngati amphamvu; akwera linga ngati anthu a nkhondo; niliyenda liri lonse njira yace, osasokonezeka m'mabande ao.
8. Sakankhana, ayenda liri lonse m'mopita mwace; akagwa m'zida, siityoka nkhondo yao.
9. Alumphira mudzi, athamanga palinga, akwerera nyumba, alowera pamazenera ngati mkhungu.