Yoswa 24:31-33 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

31. Ndipo Israyeli anatumikira Yehova masiku onse a Yoswa, ndi masiku onse a akulu akulu otsala atafa Yoswa, amene anadziwa nchito yonse ya Yehova anaicitira Israyeli.

32. Ndipo mafupa a Yosefe amene ana a Israyeli anakwera nao kucokera ku Aigupto anawaika ku Sekemu, pa kadziko kamene adakagula Yakobo kwa ana a Hamori atate wa Sekemu ndi kuwapatsa ndalama zana; ndipo anakhala colowa ca ana a Yosefe.

33. Eleazarenso mwana wa Aroni anafa; ndipo anamuika pa phiri la Pinehasi mwana wace, limene adampatsa ku mapiri a Efraimu.

Yoswa 24