1. Pamenepo Yoswa anaitana Arubeni ndi Agadi, ndi pfuko la Manase logawika pakati,
2. nanena nao, Mwasunga inu zonsezo anakulamulirani Mosemtumiki wa Yehova; mwamveranso mau anga m'zonse ndinakulamulirani inu;
3. simunasiya abale anu masiku awa ambiri mpaka lero lino, koma mwasunga cisungire lamulola Yehova Mulungu wanu.
4. Ndipo tsopano Yehova Mulungu wanu wapumitsa abale anu, monga adanena nao; potero bwererani tsopano, mu kani ku mahema anu, ku dziko la colowa canu cimene Mose mtumiki wa Yehova anakuninkhani tsidya lija la Yordano.