Yoswa 21:33-37 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

33. Midzi yonse ya Agerisoni monga mwa mabanja ao ndiyo midzi khumi ndi itatu ndi mabusa ao.

34. Ndipo anapatsa kwa mabanja a ana a Merari, otsala a Alevi, motapira pa pfuko la Zebuloni, Yokineamu ndi mabusa ace, ndi Karita ndi mabusa ace,

35. Dimna ndi mabusa ace, Nahalala ndi mabusa ace; midzi inai.

36. Ndipo motapira pa pfuko la Rubeni, Bezeri ndi mabusa ace, ndi Yahazi ndi mabusa ace,

37. Kedimotu ndi mabusa ace, ndi Mefati ndi mabusa ace; midzi inai.

Yoswa 21