20. Ndipo mabanja a ana a Kohati, Aleviwo, otsala a ana a Kohati, analandira midzi ya maere ao motapira pa pfuko la Efraimu.
21. Ndipo anawapatsa Sekemu ndi mabusa ace ku mapiri a Efraimu, ndiwo mudzi wopulumukirako wakupha mnzaceyo, ndi Gezeri ndi mabusa ace;
22. ndi Kibizaimu ndi mabusa ace, Betihoroni ndi mabusa ace; midzi inai.
23. Ndipo motapira m'pfuko La Dani, Eliteke ndi mabusa ace, Gibetoni ndi mabusa ace;
24. Aijaloni ndi mabusa ace, Gati-rimoni ndi mabusa ace; midzi inai.
25. Ndipo motapira pa pfukola Manaselogawika pakati, Taanaki ndi mabusa ace, ndi Gati-rimoni ndi mabusa ace; midzi iwiri.
26. Midzi yonse ya mabanja a ana otsala a Kohati ndiyo khumi ndi mabusa ao.