11. Ndipo maere a ana a Benjamini anakwera monga mwa mabanja ao; ndi malire a gawo lao anaturuka pakati pa ana a Yuda ndi ana a Yosefe.
12. Ndipo malire ao a kumpoto anacokera ku Yordano; ndi malire anakwera ku mbali ya Yeriko kumpoto, nakwera pakati pa mapiri kumadzulo; ndi maturukiro ace anali ku cipululu ca Beti-aveni.
13. Ndipo malire anapitirirapo kumka ku Luzi, ku mbali ya Luzi, momwemo ndi Beteli, kumwela; ndi malire anatsikira kumka ku Atarotu-adara, ku phiri lokhala kumwela kwa Betihoroni wa kunsi.