28. Ici ndi colowa ca ana a Gadi, monga mwa mabanja ao, midzi yace ndi miraga yace.
29. Mose anaperekanso colowa kwa pfuko la Manase logawika pakati, ndico ca pfuko la Manase logawika pakati monga mwa mabanja ao.
30. Ndipo malire ao anayambira ku Mahanaimu, Basana lonse, ufumu wonse wa Ogi mfumu ya ku Basana, ndi midzi yonse ya Yairi, yokhala m'Basana, midzi makumi asanu ndi limodzi;
31. ndi Gileadi logawika pakati, ndi Asitarotu ndi Edrei, midzi ya ufumu wa Ogi m'Basana, inali ya ana a Makiri mwana wa Manase, ndiwo ana a Makiri ogawika pakati, monga mwa mabanja ao.