1. Ndipo awa ndi mafumu a dzikolo amene ana a Israyeli anwakantha, nalanda dziko lao tsidya la Yordano kum'mawa, kuyambira cigwa ca Arimoni, mpaka phiri la Herimoni, ndi cidikha conse ca kum'mawa;
2. Sihoni mfumu ya Aaroori wokhala m'Hesiboni, wocita ufumu kuyambira ku Aroeri ndiwo m'mphepete mwa cigwa ca Arinoni, ndi pakati pa cigwa ndi pa Gileadi wogawika pakati, kufikira mtsinje wa Yaboki, ndiwo malire a ana a Amoni;